Sunday, January 9, 2011

MULUNGU ATATE


2.0. ZOYENERA KUDZIWA:
 Chikhalidwe cha Mulungu
 Kodi Mulungu ndi ndani?
 Ukulu wa Mulungu
 Chilengedwe
 Chimene ife tiri pamaso pa Mulungu
 Kukhulupirira Mulungu

2.1. MULUNGU ATATE.
Mulungu ndi chikondi ndipo ndi Mlengi wa zonse. Iye alibe malire. Ndi chinthu chovuta kwambiri kuti tifotokoze maonekedwe ake a Mulungu. Iye alibe chiyambi ndipo alibe mathero; amafikira dziko lonse lapansi. Ngakhale kuti Iye amakhala Kumwamba, mphamvu zake zimaonekera Kumwamba ndi dziko lonse lapansi. Ife tonse tidalengedwa ndi mphamvu zake (Yobu 11:7, Yesaya 66:1, Masalimo 139, 47:8, Genesisi 1).

2.2. CHIKHALIDWE CHA MULUNGU.

2.2.1. Woyera:
Mulungu ndiye mwini chiyero. Iye amakhala m’chiyero nthawi zonse ndipo chiyero chake chimaonekera kwa ana ake amene amachita chifuniro chake. Onse okhulupirira Mulungu magawana chiyero chake mwa Mzimu Woyera (1 Samuele 2:2, Levitiko 19:2, 2 Mbiri 20:21, Masalimo 29:2, Mateyu 5:48, 19:16-19, Aroma 11:22, 15:16, Aheberi 12:10,14, 1 Petro 1:16, Chivumbulutso 15:4).

2.1.2. Wolungama:
Mulungu sakondwera ndi machimo. Iye sakhala mu uchimo. Anthu onse omutsatira Iye akuyenera kuyenda m’chilungamo chake nthawi zonse ndi kudana nacho chinyengo chiri chonse (Yobu 34:12, Masalimo 7:9, 1 Akorinto 6:9-10, Aheberi 1:8-9, 12:4, 1 Yohane 3:7-9, Chivumbulutso 16:5, 19:2).

2.1.3. Wachikondi ndi chifundo:
Mulungu ndiye chikondi ndipo chikondicho chimayambira kwa Iye. Mwa chikondi chake anatipatsa Mwana wake kutifera pamtanda kuti tipeze chipulumutso. Iye amatichotsera mantha athu onse kuti tionane naye maso ndi maso kudzera m’Mau ake. Chifukwa cha ichi, palibe chotilekanitsa ife ndi Iye ngati tikhala mwa Iye nthawi zonse (Levitiko 19:18, Masalimo 69:16, Maliro 3:22-23, Luka 10:27, Yohane 3:16, Aroma 8:37-39, 1 Akorinto 13:4-7, Agalatiya 5:14, Aheberi 4:16).

2.1.4. Wokhulupirika ndi choonadi:
Mulungu ndi wokhulupirika nthawi zonse. Mulungu amakwaniritsa zonse zimene walonjeza popanda chokaikitsa. Iye sali ngati munthu amene kukhulupirika kwake nkokaikitsa nthawi zonse. Mulungu amakonda munthu wokhulupirika m'zochita zake ndipo amapereka madalitso ake kwa munthu wotere (Yesaya 25:1, Chivumbulutso 3:14, 19:11, Aroma 3:4, Yohane 17:3, Aheberi 10:23, 11:11, 1 Atesolonika 5:23-24, 2 Timoteo 1:12, 1 Akorinto 10:13, Masalimo 31:23, 101:6, Mateyu 25:21).

2.3. Wopereka:
Mulungu mwa chikondi chake amatipatsa ife zinthu zosiyanasiyana kuti zitithandize pamoyo wathu monga:
 Malemba onse a m’Baibulo
 Mwana wake Yesu Kristu
 Mzimu wake Woyera
 Chikhululukiro cha machimo
 Chisomo chake kwa odzichepetsa pamaso pake
 Mpumulo kwa onse olema ndi othodwa
 Nzeru zakuya za uzimu kwa ana ake
 Kupambana koposa padziko lapansi kudzera mwa Kristu
 Kuthekera koposa mu utumiki wake
 Chakudya pamoyo wathu
 Mphamvu zolamulira m’chilungamo chake. Tikhale nao mtima wothandiza anzathu mosanyinyirika ndi mopanda tsankho (Masalimo 136:25, Daniele 2:37, 2:23, Yohane 3:16, Aroma 5:5, 6:23, 8:32, 2 Timoteo 2:25, 1 Petro 4:11, 5:5, Yakobo 1:5, 4:6, 1 Akorinto 15:57, Mateyu 11:28, Luka 11:13, 1 Atesolonika 4:8, Aefeso 3:7, Deuteronomo 8:18).

2.4. UKULU WA MULUNGU.

2.4.1. Amadziwa zonse:
Nzeru za Mulungu nzodabwitsa ndipo nzovuta kuzidziwa ndi kuzimvetsa. Iye amadziwa china chiri chonse pamoyo wathu (Aroma 6:27, Yobu 9:4, 1 Samuele 2:3, Masalimo 139:4-6, Aroma 11:33, Yakobo 3:14-17, 1:5-7, Akolose 1:9, 2:2-3, 3:16, Aefeso 1:17, 1 Akorinto 3:18-20). Nzeru ndi zochita za Mulungu ndi:
 Zopanda chinyengo
 Zimabweretsa mtendere ndi chimvano
 Ziribe ukali ndi ululu
 Zachifundo ndipo zimatiululira chikondi chake osati chilamulo ai
 Ziribe kukondera kwina kuli konse
 Ziribe umadyera mphotho.

2.4.2. Amapezeka pena pali ponse:
Mulungu amapezeka pali ponse ndipo ndi chifukwa chake tikamapemphera timakhala ndi chikhulupiriro kuti zonse zimene tikupempha, zimveka kwa Iye. Palibe amene angathe kubisala kapena kuzemba pamaso pa Mulungu. Ngakhale Iye amapezeka pali ponse, sizikutanthauza kuti amapezekanso mu zinthu zonse ai. Mu zinthu monga izi, Iye sapezekamo:

 Mafano kapena kupembedza Mdierekezi (Yesaya 2:8-11, 20-21, Chivumbulutso 9:20)
 Kupembedza chilengedwe kapena zolengedwa zina (Aroma 1:25).
 Kupembedza Angelo (Akolose 2:18, Chivumbulutso 22:8-9).
 Kupembedza mizimu ya anthu akufa (Levitiko 20:6, Deuteronomo 18:9-11, Yesaya 8:19).

2.4.3. Wamphamvu zonse:
 Iye ndiye Mlengi wa kumwamba ndi dziko (Genesisi 1).
 Mwa Iye, zinthu zonse zidalengedwa ndipo zidakhazikika (Akolose 1:17).
 Mphamvu zake nzochuluka (Yobu 9:4).
 Zinthu zonse ndi zotheka ndi Mulungu (Mateyu 19:26, Yeremia 32:17, 27, 1 Akorinto 1:25, Yoele 3:10, 2 Akorinto 12:10, Aheberi 11:34).

2.4.4. Wamuyaya:
Mulungu alibe malire ndipo adzakhala mpaka muyaya. Iye ndi Woyamba ndi Wotsiriza. Iye adali, ali ndipo adzakhala mpaka nthawi zosatha (Yesaya 43:10, Yohane 3:15-16, Aroma 6:23, 1 Yohane 5:11-13, 20, 2 Timoteo 1:12, Masalimo 90:1-2, Chivumbulutso 22:1-8).

2.4.5. Samasintha:
Mulungu ali yemweyo nthawi zonse kotero chikondi chake nchosathanso. Nkoyenera kumkhulupirira ndi kumudalira nthawi zonse (1 Akorinto 15:51-53, Aheberi 13:8, Yakobo 1:17, 1 Yohane 3:2).

2.5. CHILENGEDWE.

2.5.1. Tsiku Loyamba:
Patsiku loyamba Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi lidali lopanda maonekedwe eni eni ndiponso losakonzeka. M’dima udali utaphimba nyanja yaikulu ponse ponse ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. Mulungu adalamula kuti kuyere ndipo kudatero ndipo kuyerako ndiko masana ndi m’dima ndiwo usiku. Kudali madzulo ndiponso m’mawa pa tsiku loyamba.

2.5.2. Tsiku Lachiwiri:
Mulungu adalekanitsa madzi kuti akhale pa malo awiri olekana. Adalenga cholekanitsa madzi ndipo dzina lake ndilo thambo.

2.5.3. Tsiku Lachitatu:
Mulungu adaika madzi pamalo amodzi kuti mtunda uoneke. Mtundawo ndilo dziko lapansi. Madzi osonkhanitsidwa pamodzi aja ndiwo nyanja. Panthaka padamera zomera zobala njere ndi mitengo yobala zipatso zanjere monga mwa mtundu wake. Padziko padamera zipatso za mitundu yonse.

2.5.4. Tsiku Lachinai:
Mulungu adalenga kuthambo kuti kukhale miyuni iwiri ikulu ikulu kulekanitsa usana ndi usiku. Iyo, idali zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka. Muuni waukulu wowala masana adautcha dzina lake dzuwa ndipo wowala usiku Mwezi. Iye adalenganso nyenyezi za kuthambo.

2.5.5. Tsiku Lachisanu:
M’nyanja mudali zamoyo zambirimbiri komanso mbalame zouluka mlengalenga. M’nyanja mudali nsomba zazikulu pamodzi ndi zolengedwa zina zokhala m’madzi ndiponso mbalame ndi zouluka zina za mitundu mitundu.

2.5.6. Tsiku Lachisanu ndi chimodzi:
Padali mitundu yonse ya zamoyo monga zoweta, zokwawa, ndi nyama zakuthengo potsata mitundu yake. Mulungu adalenga munthu m’chifanizo chake kuti alamulire zolengedwa zonse.

2.5.7. Tsiku Lachisanu ndi chiwiri:
Mulungu adamaliza kulenga zinthu zonse ndipo adapuma. Iye adalidalitsa tsiku limeneli, naliyeretsa chifukwa patsikuli adapuma atatsiriza kulenga zinthu zonse.

2.6. CHIMENE IFE TIRI PAMASO PA MULUNGU.
 Ndife olengedwa ake a Mulungu (Masalimo 139:14-16).
 Ndife ake eni eni a Mulungu (1 Akorinto 6:19-20).
 Ndife oitanidwa kuti timpembedze Mulungu (Chivumbulutso 4:11).

2.7. CHISANKHO CHATHU.
Yesu Kristu adati: “Kondani Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi nzeru zanu zonse ndi mphamvu zanu zonse“(Mateyu 22:37). Munthu adalengedwa kuti atumikire ndi kukonda Mulungu nthawi zonse. Baibulo limatiuza za Yoswa amene adali mtsogoleri wa Aisraeli. Iyeyu adali munthu wamphamvu pa utumiki wake ndipo adatsogolera Aisraeli ndi kupambana nkhondo zimene ankamenyana ndi adani awo. Yoswa adauza Aisraeli kuti adzisankhire okha womtumikira koma iye ndi banja lake adasankha kutumikira Mulungu ngakhale zinthu zitavuta bwanji (Yoswa 24:15). Lero lino chisankho chimenechi chikubwera kwa ife. Kodi timdzamtumikira Mulungu kapena zochita zathu zikutilekanitsa ife kuyandikana naye Atate wathu.


Download Pdf version from here!

God Bless you!

No comments:

Post a Comment