Sunday, January 9, 2011

BAIBULO


1.1.1. ZOYENERA KUDZIWA:
 Baibulo ndi chiani
 Cholinga cha Baibulo
 Zimene Baibulo limafotokoza
 Amene adalemba Baibulo
 Mwini wake Baibulo
 Kufunika kwa Baibulo
 Oyenera kuwerenga ndi kugwiritsa ntchito Baibulo
 Chiyembekezo cha Mkristu

1.1.2. KODI BAIBULO NDI CHIANI?
Baibulo ndi Mau a Mulungu ndipo ndi Bukhu Lopatulika kwambiri pa mabuku onse. Bukhuli lidalembedwa ndi anthu osiyanasiyana amene adatsogozedwa ndi Mzimu Woyera (2 Timoteo 3:16). Ngakhale Baibulo liri mabukhu okwana 66 mkati mwake, mutu wake ndi umodzi basi: “Chikonzero cha Mulungu chopulumutsa dziko lapansi”. Bukhuli liri ndi zigawo ziwiri: “Chipangano Chakale ndi Chiangano Chatsopano”. Chipangano Chakale chiri ndi mabuku 39 ndipo Chipangano Chatsopano chiri ndi 27 potsatira Bukhu limene lalembedwa kuti: “Bukhu Lopatulika- Mulungu Anena Masiku Ano”.

1.1.3. LONJEZO LOPAMBANA.
Lonjezo lopambana limene Baibulo limatiululira ndi Moyo Wosatha kudzera mwa Mwana wake Yesu Kristu. Mulungu adalonjeza Moyo Wosatha ngati tikhulupirira Yesu Kristu kukhala Mbuye ndi Mpulumutsi wa moyo wathu nthawi zonse (Yohane 3:16).

1.1.4. CHOLINGA CHA BAIBULO.
Cholinga cha Mau a Mulungu kwa ife ndi kufuna kutiunikira njira yopita kumwamba kwa Atate. Mau a Mulungu ali pakati pathu kutidzudzula, kutikonza, kutiphunzitsa ndi kutipatsa nzeru zochuluka zakuya mu uzimu kuti chikhulupiriro chathu mwa Kristu chikule koposa (2 Timoteo 3:15-16, 2 Petro 1:3-4).

1.1.5. KUWERENGA BAIBULO.

Tiyenera kuwerenga Baibulo pa zifukwa izi:

1.1.5.1. Kuti tikule mu Uzimu:
Mau a Mulungu ndi chakudya chimene chimapereka thanzi ku moyo wathu kuti tikule ndi nzeru zoopa Mulungu nthawi zonse ndipo moyo wathu umakhala wokhathamira ndi madalitso ake pamene tisunga ndi kugwiritsa ntchito Mau ake m’moyo wathu (Yeremia 15:16, Ezekiele 3:1-3, 1 Petro 2:2, 1 Akorinto 3:1-2, Aheberi 5:12-14).

1.1.5.2. Kuti tipewe machimo:
Mau a Mulungu amatitsogolera ife ku njira yoongoka pamaso pa Mulungu ndipo amabweretsa chiyero pakati pathu kuti tipewe machimo ndi machenjerero a Satana woipayo (Masalimo 119:9-11,133, Yesaya 59:1).

1.1.5.3. Kuti tikhale ndi moyo wabwino ndi thanzi:
Kumvera Mau a Mulungu kumachititsa kuti munthu akhale ndi moyo wabwino komanso kuchira kumatenda aku thupi ndi uzimu (Eksodo 15:26, Masalimo 107:20, 119:50).

1.1.5.4. Kuti tikhale ndi chuma choposa:
Mulungu adalonjeza kukhala ndi moyo wosasowa kanthu m’moyo wathu wa uzimu ngati timutsatira Iye m’choonadi. Tiyenera kuwerenga Mau ake kuti tidziwe ndi kupeza chuma cha mtengo wa patari chimene Mulungu watisungira pochita chifuniro chake (Yoswa 1:8, Masalimo 1:1-3).

1.1.5.5. Kuti tithandizike popemphera:
Mau a Mulungu ndi chida chathu chimene timagwiritsa ntchito popemphera pamaso pake kuti tisasowe chomuuza (Yohane 15:7).

1.1.5.6. Kuti tipeze mphamvu:
Mau a Mulungu amamanga makoma olimba m’mitima yathu kuti ngakhale zopsinja ndi zotibwezeretsa m’mbuyo zambiri tikumane nazo, tipitebe mtsogolo ndi Chikhulupiriro chathu mwa Mulungu Atate kudzera mwa Mwana wake Yesu Kristu (Mateyu 7:24).

1.1.5.7. Kuti tipeze moyo:
Mau a Mulungu amapereka moyo kwa iwo amene ali akufa mu uzimu kuti atsitsimuke ndi kufika mu ufumu wa Mulungu (Yohane 6:63, Masalimo 33:6,9, Aheberi 11:3).

1.1.7. KODI MU BAIBULO MULI ZOLAKWITSA ZINA ZIRIZONSE?
Baibulo ndi Bukhu Lopatulika pa mabuku onse amene tingawapeze pa dziko lonse la pansi. Mzimu Woyera wa Mulungu anatsogolera atumiki ake osiyanasiyana kuti alembe Bikhuli popanda cholakwitsa china chiri chonse. Mulungu kudzera mwa Mzimu Woyera anatsogolera atumiki amenewa kuti:
 Alembe zokhazo zimene Mulungu anawaunikira kuti alembe
 Alembe Mau onse m’Bukhuli popanda zolakwitsa.

Mulungu mwini wake ndiye amene amateteza mau ake kuti asaonongeke m’njira ina iriyonse. Ichi ndi chifukwa chake anthu onse oomboledwa ndi mwazi wa Kristu amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mau eni eni ochokera kwa Mulungu (Yesaya 27:3, 40:8, Mateyu 5:18, 24:35, Yohane 10:35).

1.1.8. MAU A MULUNGU (BAIBULO) AMAFANIZIDWA NDI:

1.1.8.1. Madzi:
Mau a Mulungu amatiyeretsa ndi kutisunga kuti tikhale oyera nthawi zonse. Tikachita chisankho m’moyo wathu kutumikira ndi kuchita chifuniro cha Mulungu, Iye amatiyeretsa ndi kutiteteza ku machismo (Yohane 15:3, Aefeso 5:22-27, Masalimo 119:9-11).

1.1.8.2. Kuwala:
Mau a Mulungu ndi nyale ndipo amatiunikira njira yathu kuti tisayende mumdima wa imfa kotero kuti amatipatsa chidziwitso kuti tisalowe mu uchimo (2 Petro 1:9, Masalimo 119:105, 130).

1.1.8.3. Chakudya:
Mau a Mulungu ndi chakudya cha moyo wathu wa uzimu kuti tikule ndi thanzi lolemekeza ndi kutumikira Mulungu nthawi zones (1 Akorinto 3:1-2, 1 Petro 2:2. Aefeso 4:12-15, Yohane 6:20).

1.1.8.4. Mbeu:
Mau a Mulungu ndi mbeu imene ikalowa ndi kukhazikika mkati mwa mtima wathu, imakula ndi kubereka zipatso za uzimu pamaso pa Mulungu. Pa chifukwa ichi, moyo wathu umakhala wopindulitsa koposa pamaso pa Mulungu (Luka 8:14-15, Masalimo 1:3, 2 Akorinto 9:10, 1 Petro 1:23).

1.1.8.5. Lupanga:
Mau a Mulungu ndi Lupanga komanso chida cholimba chothamangitsira nacho Satana. Mwachitsanzo, Kristu adagwiritsa ntchito Mau a Mulungu pogonjetsa Satana m’chipululu muja (Luka 4:1-14, Aefeso 6:17, Aheberi 4:12).

1.1.8.6. Moto:
Mau a Mulungu amaotcha maganizo ndi malingaliro oipa ndipo amatiunikira kuti tikule ndi malingaliro amene achitira ubwino dzina la Mulungu wathu (Yeremia 23:29).

1.1.8.7. Mkaka:
Mau a Mulungu amapereka thanzi kuti tikule ndi moyo wokhathamira ndi madalitso a Mulungu ndiponso moyo wopanda nkhawa ndi mavuto a dziko lapansi (1 Petro 2:2).

1.1.8.8. Uchi:
Mau Mulungu amakoma ngati uchi tikamawerenga chifukwa nthawi ndi nthawi amativumbulutsira zinsinsi zatsopano pa moyo wathu wa uzimu (Masalimo 19:10).

1.1.8.9. Golide:
Mau a Mulungu ndi chuma choposa zina zonse chimene chimapezeka ngati munthu akhulupirira Yesu Kristu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi wa moyo wake (Yeremia 19:10).

1.1.8.10. Kalilole (Galasi):
Mau a Mulungu limationetsa chithunzithunzi cha ufumu wa Kumwamba tikatsegula maso ndi mitima yathu kuti Mau’wo akhale mkati mwathu. Amationetseranso malonjezo oposa amene Mulungu watiikira pa moyo wathu (Yakobo 1:23-25).

1.1.8.11. Nyundo (Hamala):
Mau ake Mulungu amaswa makoma onse a uchimo amene ali mkati mwathu ndipo amatithandizanso kuti tiswe malingaliro oipa mkati mwathu (Yeremia 23:29).

1.1.9. MAGAWO AMENE BAIBULO LAFUNGATIRA:

1.1.9.1. Chilamulo:
Mabuku a chilamulo ndi mabuku asanu oyambirira m’Chipangano Chakale kuyamba ndi Genesisi mpaka Deuteronomo. Mulungu adapereka Malamulo osiyanasiyana okhudza moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Choncho, kuwerenga ndi kumvetsa Malamulo ake kungapindulutse miyoyo yathu pamaso pa Mulungu.

1.1.9.2. Mbiri:
Mbiri ndi nkhani kapena zochitika zikulu zikulu zochititsa chidwi zimene zimachitika pa moyo wathu watsiku ndi tsiku. Baibulo limafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zidachitika kuti ife titengepo phunziro. Mabuku ofotokoza mbiri m’Chipangano Chakale ndi Yoswa mpaka Estere ndipo m’Chipangano Chatsopano ndi Mateyu mpaka Machitidwe a Atumwi.

1.1.9.3. Luntha:
Luntha ndi chimangiriro cha luso ndi nzeru zoposa zimene Mulungu adationetsera kudzera mwa atumiki ake osiyanasiyana kuti tiphunzire ndi kutakasidwa m’mitima yathu pamaso pake. Mabuku amene amafotokoza za luntha ndi Yobu mpaka Nyimbo ya Solomo m’Chipangano Chakale.

1.1.9.4. Ulosi:
Mabuku a Ulosi ndi Yesaya mpaka Malaki m’Chipangano Chakale. Mchipangano Chatsopano bukhu la Chivumbulutso komanso magawo ena a mabuku a Mateyu, Mariko, Luka ndi Yohane ali ndi mau a ulosi. Mabuku amenewa amatiphunzitsa ndi kutiululira chikonzero cha Mulungu pamoyo wathu watsopano ndi mtsogolo (Chivumbulutso 20:4, 1 Akorinto 6:2).

1.1.9.5. Chikhalidwe:
Baibulo limationetsa chikhalidwe chabwino chimene tingatsatire pamoyo wathu. Izi zikuonetsedwa kwambiri m’Chipangano Chatsopano komanso m’mabuku ena m’Chipangano Chakale monga Miyambo ndi Mlaliki.

1.2.0. KUDZIWA ZIMENE BAIBULO LIKUPHUNZITSA.
Poyamba peni peni tikuyenera kudziwa kuti Mau onse opezeka m’Baibulo adalembedwa kuti ife tikhulupirire kuti Yesu Kristu ndiye Wolonjezedwa uja ndipo zonse zidalembedwa kumuchitira Iye umboni (Yohane 20:31, Luka 24:44). Tingadziwe zimene Baibulo likuphunzitsa kudzera m’njira monga izi:

1.2.0.1. Kudzera m’mavumbulutso a Mzimu Woyera:
 Pezani nthawi yabwino yoti muthe kukhala pansi ndikulingalira Mau a Mulungu.
 Funsani Mzimu Woyera kuti akuphunzitseni ndi kudzodza koyenera (Yohane 14:26, 1 Akorinto 2:12-14, 
    Yohane 2:27).
 Pempherani kuti zotchinga za Woipayo zichoke m’moyo wanu kuti mukhale ndi chidziwitso pa Mau ake (2 
    Akorinto 3:14-16).
 Pempherani kuti Mzimu Woyera akupatseni ndi kutsegula chidziwitso chanu (Luka 24:25-27,44-45).
 Pempherani kuti Mzimu wachidziwitso ndi nzeru zoposa komanso mavumbulutso akhale pa inu pamene 
    mukuwerenga Baibulo lanu (Aefeso 1:17-19).

1.2.0.2. Kuwerenga Mau a Mulungu nthawi ndi nthawi:
 Pezani nthawi yosachepera mphindi 30 tsiku ndi tsiku kuti muwerenge Baibulo.
 Werengani Salimo imodzi patsiku ndipo mudzakhala mutawerenga Masalimo onse kawiri pachaka.
 Werengani mutu umodzi m’bukhu la Miyambo patsiku ndipo mudzakhala mutawerenga bukhu lonse la 
    Miyambo kamodzi pamwezi.
 Werengani masamba atatu m’Chipangano Chakale patsiku ndipo mudzakhala mutawerenga Chipangano 
    chonse Chakale kamodzi pachaka.
 Werengani masamba atatu patsiku m’Chipangano Chatsopano ndipo mudzakhala mutawernga Chipangano 
     chonse katatu pachaka.
 Nthawi imene mungasankhe kuwerenga Baibulo lanu ilibe kanthu kweni kweni koma m’mamawa ndi 
    madzulo ndiye nthawi zimene bongo wa munthu umakhala wokonzeka Kulandira zinthu (Masalimo 3:5, 
   4:8).
 Werengani Baibulo lanu mofatsa ndi mosamalitsa. Musathamange. Lingalirani zonse zimene mukuwerenga 
     bwino lomwe.
 Pempherani kwa Mulungu kuti akuunikireni zonse zimene mukufuna kuti mudziwe kuchoka m’Baibulo. 
    Palibe wina amene angamasulire Baibulo momveka bwino kuposa Mulungu mwini wake.
 Powerenga lolani kuti Mulungu akulankhuleni mkati mwa mtima wanu. Dziwani kuti Baibulo lidalembedwa 
    kwa inu. Ngati pali uthenga, uthengawo ukupita kwa inu. Ngati pali chenjezo, chenjezolo likupita kwa inu 
    osati munthu wina ai. Chimodzomodzinso lonjezo kuti zikuchitireni inu ubwino wonse (Agalatiya 2:20).
 Mukatsiriza kuwerenga, pempherani kuti Mulungu amangirire zonse mkati mwa mtima wanu. Sungani 
    pamtima magawo amene akukhudzani kwambiri ndipo muwalingalire mozama. Mulungu adzakudalitsani 
    koposa (Masalimo 119:11).




God bless you!

No comments:

Post a Comment